Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

ZEKARIYA 9

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Mawu a Yehova odzudzula dziko la Hadiraki ndi mzinda wa Damasiko pakuti maso a anthu ndiponso mafuko onse a Israeli ali pa Yehova—
2ndiponso mzinda wa Hamati, umene ukuchita malire ndi dzikoli, komanso pa Turo ndi Sidoni, ngakhale kuti iwo ndi anzeru kwambiri.
3Ndipo Turo anadzimangira linga; wadziwunjikira siliva ngati fumbi, ndi golide ngati zinyalala za mʼmisewu.
4Taonani Ambuye adzamulanda chuma chakecho ndi kuwononga mphamvu zake mʼnyanja, ndipo adzapserera ndi moto.
5Mzinda wa Asikeloni udzaona zimenezi, nʼkuchita mantha; Gaza adzanjenjemera ndi ululu, chimodzimodzinso Ekroni, chifukwa chiyembekezo chake chidzatheratu. Mfumu ya ku Gaza idzaphedwa ndipo Asikeloni adzakhala opanda anthu.
6Mu Asidodi mudzakhala mlendo, ndipo ndidzathetsa kunyada kwa Afilisti.
7Ndidzachotsa nyama ya magazi mʼkamwa mwawo, chakudya choletsedwa mʼmano mwawo. Amene atsala adzakhala anthu a Mulungu wathu, adzasanduka atsogoleri mu Yuda, ndipo Ekroni adzakhala ngati Ayebusi.
8Koma Ine ndidzalondera Nyumba yanga ndi kuyiteteza kwa ankhondo osakaza. Palibenso mdani amene adzagonjetse anthu anga, pakuti tsopano ndikuwayangʼanira.
9Sangalala kwambiri, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni! Fuwula, mwana wamkazi wa Yerusalemu! Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe, yolungama ndi yogonjetsa adani, yodzichepetsa ndi yokwera pa bulu, pa mwana wamphongo wa bulu.
10Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efereimu ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu, ndipo uta wankhondo udzathyoka. Mfumuyo idzabweretsa mtendere pakati pa mitundu ya anthu. Ulamuliro wake udzayambira ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, ndipo kuchokera ku Mtsinje (Yufurate) mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
11Tsono kunena za iwe, chifukwa cha magazi a pangano lako ndi Ine, ndidzamasula amʼndende ako, ndidzawatulutsa mʼdzenje lopanda madzi.
12Bwererani ku malo anu otetezedwa, inu amʼndende achiyembekezo; ngakhale tsopano ndikulengeza kuti ndidzakubwezerani zabwino mowirikiza.
13Ndidzakoka Yuda monga ndimakokera uta wanga, ndipo Efereimu ndiye muvi wake. Ndidzadzutsa ana ako iwe Ziyoni, kulimbana ndi ana ako iwe Grisi, ndipo ndidzakusandutsa iwe lupanga la munthu wankhondo.
14Pamenepo Yehova adzaonekera kwa anthu ake; mivi yake idzangʼanima ngati chingʼaningʼani. Ambuye Yehova adzaliza lipenga; ndipo adzayenda mu mkuntho wochokera kummwera,
15ndipo Yehova Wamphamvuzonse adzawateteza. Iwo adzawononga ndipo adzagonjetsa ndi miyala ya legeni. Adzamwa magazi ndi kubangula ngati amwa vinyo; magazi adzayenderera ngati a mʼmbale yowazira magazi pa ngodya za guwa lansembe.
16Tsiku limenelo Yehova Mulungu wawo adzawapulumutsa pakuti anthu ake ali ngati nkhosa. Adzanyezimira mʼdziko lake ngati miyala yokongola pa chipewa chaufumu.
17Taonani chikoka ndi kukongola kwawo! Tirigu adzasangalatsa anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.