Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

ZEKARIYA 10

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Pemphani mvula kwa Yehova pa nthawi yamphukira; ndi Yehova amene amapanga mitambo ya mvula. Iye amagwetsa mivumbi ya mvula kwa anthu, ndi kumeretsa mbewu za mʼmunda kwa aliyense.
2Mafano amayankhula zachinyengo, owombeza mawula amaona masomphenya abodza; amafotokoza maloto onama, amapereka chitonthozo chopandapake. Choncho anthu amangoyendayenda ngati nkhosa zozunzika chifukwa chosowa mʼbusa.
3“Ine ndawakwiyira kwambiri abusa, ndipo ndidzalanga atsogoleri; pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzasamalira nkhosa zake, nyumba ya Yuda, ndi kuwasandutsa ngati akavalo aulemerero ankhondo.
4Mu Yuda mudzachokera mwala wapangodya, mudzachokera chikhomo cha tenti, mudzachokera uta wankhondo, mudzachokera mtsogoleri aliyense.
5Onse pamodzi adzakhala ngati ngwazi zankhondo zoponda mʼmatope a mʼmisewu nthawi yankhondo. Chifukwa Yehova adzakhala nawo, adzachita nkhondo ndi kugonjetsa okwera pa akavalo.
6“Ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda ndi kupulumutsa nyumba ya Yosefe. Ndidzawabwezeretsa chifukwa ndawamvera chisoni. Adzakhala ngati kuti sindinawakane, chifukwa ndine Yehova Mulungu wawo ndipo ndidzawayankha.
7Aefereimu adzakhala ngati ankhondo amphamvu adzasangalala ngati anthu amene amwa vinyo. Ana awo adzaziona zimenezi ndipo adzasangalala; mʼmitima mwawo adzakondwa mwa Ambuye.
8Ndidzaliza mluzu ndi kuwasonkhanitsa pamodzi. Ndithu ndawawombola; adzachulukana ngati poyamba paja.
9Ndinawamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu, koma ku mayiko akutaliwo adzandikumbukira. Iwo pamodzi ndi ana awo adzapulumuka, ndipo adzabwerera.
10Ndidzawabweretsa kuchokera ku Igupto ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya. Ndidzawabwezera ku Giliyadi ndi ku Lebanoni, mpaka malo woti nʼkukhalamo adzatheratu.
11Adzawoloka nyanja ya masautso; nyanja yokokoma idzagonja ndipo madzi onse a mu Nailo adzaphwa. Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha ndipo ndodo yaufumu ya Igupto idzathyoka.
12Ndidzalimbitsa iwo mwa Yehova ndipo adzayenda mʼdzina lake,” akutero Yehova.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.