Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

NYIMBO YA SOLOMONI 7

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Iwe namwali waufumu, mapazi ako ngokongola mu nsapato wavalazo! Ntchafu zako nʼzowumbika bwino ngati miyala yamtengowapatali, ntchito ya manja ya mmisiri waluso.
2Mchombo wako uli ngati chikho chowumbika bwino chimene nthawi zonse ndi chodzaza ndi vinyo. Chiwuno chako ndi choningʼa ngati mtolo wa tirigu utazunguliridwa ndi maluwa okongola.
3Mawere ako akuoneka ngati ana awiri a mbawala, ngati mphoyo zamapasa.
4Khosi lako lili see! ngati nsanja ya mnyanga wa njovu. Maso ako ali ngati mayiwe a ku Hesiboni, amene ali pafupi ndi chipata cha Bati Rabimu. Mphuno yako ili ngati nsanja ya ku Lebanoni, yoyangʼana ku Damasiko.
5Mutu wako uli bwinobwino nengʼaa ngati phiri la Karimeli. Tsitsi lako lili ngati nsalu yakuda yaufumu; mfumu yakopeka ndi maonekedwe ake okongola.
6Ndiwe wokongola kwambiri ndiponso wosangalatsa, iwe wokondedwa, namwali wokondweretsawe!
7Msinkhu wako uli ngati mtengo wa mgwalangwa, ndipo mawere ako ali ngati phava la zipatso.
8Ndinati, “Ndikwera mtengo wa mgwalangwa; ndidzathyola zipatso zake.” Mawere ako ali ngati maphava a mphesa, fungo la mpweya wako lili ngati ma apulosi,
9ndipo pakamwa pako pali ngati vinyo wokoma kwambiri. Tsono vinyo ameneyu amuthirire wachikondi wanga, ayenderere bwino pa milomo yake ndi mano ake.
10Wokondedwayo ine ndine wake, ndipo chilakolako chake chili pa ine.
11Bwera wachikondi wanga, tiye tipite ku madera a ku midzi, tikagone ku midzi.
12Tiye tilawirire mmamawa kupita ku minda ya mpesa, tikaone ngati mitengo ya mpesa yayamba kuphukira, ngati maluwa ake ayamba kuoneka, komanso ngati makangadza ayamba kuonetsa maluwa. Kumeneko ndidzakuonetsa chikondi changa.
13Mitengo ya mankhwala a chisulo ikupereka fungo lake labwino, ndipo pa khomo pathu pali zipatso zonse zokoma, zatsopano ndi zakale zomwe, zimene ndakusungira wokondedwa wanga.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.