Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

NYIMBO YA SOLOMONI 6

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Iwe wokongola kuposa akazi onsewa, kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti? Kodi wokondedwa wakoyo wakhotera njira iti kuti timufunefune pamodzi ndi iwe?
2Wachikondi wanga watsikira ku munda kwake, ku timinda ta zokometsera zakudya, akukadyetsa ziweto zake ku minda, ndiponso akuthyola maluwa okongola.
3Wokondedwa wangayo ndine wake ndipo iyeyo ndi wangawanga; amadyetsa ziweto zake pakati pa maluwa okongola.
4Ndiwe wokongola, bwenzi langa, ngati Tiriza, wokongola kwambiri ngati Yerusalemu, ndiwe woopsa ngati gulu lankhondo lonyamula mbendera.
5Usandipenyetsetse; pakuti maso ako amanditenga mtima. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
6Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zimene zikubwera kuchokera kokazisambitsa, iliyonse ili ndi ana amapasa, palibe imene ili yokha.
7Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutu, masaya ako ali ngati mabandu a makangadza.
8Ngakhale patakhala akazi a mfumu 60, ndi azikazi 80, ndi anamwali osawerengeka;
9koma nkhunda yanga, wangwiro wanga ndi wosiyana ndi wina aliyense; mwana wamkazi yekhayo wa amayi ake, mwana wapamtima wa amene anamubereka. Anamwali anamuona ndipo anamutcha wodala; akazi a mfumu ndi azikazi anamutamanda.
10Ndani uyu akuoneka ngati mʼbandakucha, wokongola ngati mwezi, wowala ngati dzuwa, wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili mʼmanja?
11Ndinatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi kukayangʼana zomera zatsopano ku chigwa, kukaona ngati mpesa waphukira kapena ngati makangadza ali ndi maluwa.
12Ndisanazindikire kanthu, ndinakhala ngati ndikulota kuti ndili mʼgaleta pambali pa mfumu yanga.
13Bwerera, bwerera iwe namwali wa ku Sulami; bwerera, bwerera kuti ife tidzakupenyetsetse iwe! Chifukwa chiyani mukufuna kudzapenyetsetsa ine mwana wamkazi wa ku Sulami, pamene ndikuvina pakati pa magulu awiri?
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.