Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 66

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!
2Imbani ulemerero wa dzina lake; kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.
3Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu! Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.
4Dziko lonse lapansi limaweramira inu; limayimba matamando kwa Inu; limayimba matamando pa dzina lanu.” Sela.
5Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.
6Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma, iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi. Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.
7Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina. Anthu owukira asadzitukumule.
8Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu, mulole kuti mawu a matamando ake amveke;
9Iye watchinjiriza miyoyo yathu ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.
10Pakuti Inu Mulungu munatiyesa; munatiyenga ngati siliva.
11Inu mwatilowetsa mʼndende ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.
12Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu; ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi, koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.
13Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza ndi kukwaniritsa malumbiro anga.
14Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto.
15Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu ndi chopereka cha nkhosa zazimuna; ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi. Sela
16Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu. Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.
17Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga, matamando ake anali pa lilime panga.
18Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga Ambuye sakanamvera;
19koma ndithu Mulungu wamvetsera ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga.
20Matamando akhale kwa Mulungu amene sanakane pemphero langa kapena kuletsa chikondi chake pa ine!
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.