Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 65

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Matamando akudikira Inu Mulungu mu Ziyoni; kwa inu malumbiro athu adzakwaniritsidwa.
2Inu amene mumamva pemphero, kwa inu anthu onse adzafika.
3Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo, Inu munakhululukira mphulupulu zathu.
4Odala iwo amene inu muwasankha ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu! Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu, za mʼNyumba yanu yoyera.
5Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,
6amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu, mutadziveka nokha ndi mphamvu.
7Amene munakhalitsa bata nyanja kukokoma kwa mafunde ake, ndi phokoso la anthu a mitundu ina.
8Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu; kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera. Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.
9Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira; Inuyo mumalilemeretsa kwambiri. Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi kuti upereke tirigu kwa anthu, pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.
10Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake, mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.
11Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka, ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka.
12Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira; mapiri avekedwa ndi chisangalalo.
13Madambo akutidwa ndi zoweta ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu; izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.