Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 57

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo, pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo. Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu mpaka chiwonongeko chitapita.
2Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba, kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.
3Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa, kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri. Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.
4Ine ndili pakati pa mikango, ndagona pakati pa zirombo zolusa; anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi, malilime awo ndi malupanga akuthwa.
5Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba; mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.
6Iwo anatchera mapazi anga ukonde ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa. Anakumba dzenje mʼnjira yanga koma agweramo okha mʼmenemo.
7Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu mtima wanga ndi wokhazikika. Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.
8Dzuka moyo wanga! Dzukani zeze ndi pangwe! Ndidzadzuka mʼbandakucha.
9Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko.
10Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba; kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo.
11Mukwezekedwe Inu Mulungu kuposa mayiko akumwamba, mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.