Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 56

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Mundichitire chifundo Inu Mulungu, pakuti anthu akundithamangitsa kwambiri; tsiku lonse akundithira nkhondo.
2Ondinyoza akundithamangitsa tsiku lonse, ambiri akumenyana nane monyada.
3Ndikachita mantha ndimadalira Inu.
4Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda, mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha. Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?
5Tsiku lonse amatembenuza mawu anga; nthawi zonse amakonza zondivulaza.
6Iwo amakambirana, amandibisalira, amayangʼanitsitsa mayendedwe anga ndipo amakhala ndi chidwi chofuna kuchotsa moyo wanga.
7Musalole konse kuti athawe; mu mkwiyo wanu Mulungu mugwetse mitundu ya anthu.
8Mulembe za kulira kwanga, mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu. Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo?
9Adani anga adzabwerera mʼmbuyo pamene ndidzalirira kwa Inu. Pamenepo ndidzadziwa kuti Mulungu ali ku mbali yanga.
10Mwa Mulungu amene mawu ake ndimawatamanda, mwa Yehova amene mawu ake ndimawatamanda,
11mwa Mulungu ine ndimadalira ndipo sindidzachita mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
12Ndiyenera kuchita zomwe ndinalumbira kwa Mulungu; ndidzapereka nsembe zanga zachiyamiko kwa inu.
13Pakuti mwawombola moyo wanga ku imfa ndi mapazi anga kuti ndingagwe, kuti ndiyende pamaso pa Mulungu mʼkuwala kwa moyo.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.