Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

ZEFANIYA 2

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Sonkhanani pamodzi, sonkhanani pamodzi, inu mtundu wochititsa manyazi,
2isanafike nthawi yachiweruzo, nthawi yanu isanawuluke ngati mungu, usanakufikeni mkwiyo woopsa wa Yehova, tsiku la ukali wa Yehova lisanafike pa inu.
3Funafunani Yehova, inu nonse odzichepetsa a mʼdziko, inu amene mumachita zimene amakulamulani. Funafunani chilungamo, funafunani kudzichepetsa; mwina mudzatetezedwa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.
4Gaza adzasiyidwa ndipo Asikeloni adzasanduka bwinja. Nthawi yamasana Asidodi adzakhala wopanda anthu ndipo Ekroni adzazulidwa.
5Tsoka inu okhala mʼmbali mwa nyanja, inu mtundu wa Akereti; mawu a Yehova akutsutsa iwe Kanaani, dziko la Afilisti. “Ndidzakuwononga ndipo palibe amene adzatsale.”
6Dziko la mʼmbali mwa nyanja, kumene kumakhala Akereti, lidzakhala malo a abusa ndi la makola a nkhosa.
7Malowa adzakhala a anthu otsala a nyumba ya Yuda; adzapezako msipu. Nthawi ya madzulo adzagona mʼnyumba za Asikeloni. Yehova Mulungu wawo adzawasamalira; adzabwezeretsa mtendere wawo.
8“Ndamva kunyoza kwa Mowabu ndi chipongwe cha Amoni, amene ananyoza anthu anga ndi kuopseza kuti alanda dziko lawo.
9Choncho, pali Ine Wamoyo,” akutero Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, “Ndithu, Mowabu adzasanduka ngati Sodomu, Amoni adzasanduka ngati Gomora; malo a zomeramera ndi maenje a mchere, dziko la bwinja mpaka muyaya. Anthu anga otsala adzawafunkha; opulumuka a mtundu wanga adzalandira dziko lawo.”
10Ichi ndi chimene adzalandire chifukwa cha kunyada kwawo, chifukwa chonyoza ndi kuchitira chipongwe anthu a Yehova Wamphamvuzonse.
11Yehova adzawachititsa mantha kwambiri pamene adzawononga milungu yonse ya mʼdzikomo. Ndipo mitundu ya anthu pa dziko lonse idzamulambira, uliwonse ku dziko la kwawo.
12“Inunso anthu a ku Kusi, mudzaphedwa ndi lupanga.”
13Yehova adzatambasulira dzanja lake kumpoto ndi kuwononga Asiriya, kusiya Ninive atawonongekeratu ndi owuma ngati chipululu.
14Nkhosa ndi ngʼombe zidzagona pansi kumeneko, pamodzi ndi nyama zakuthengo za mtundu uliwonse. Akadzidzi a mʼchipululu ndi akanungu adzakhala pa nsanamira zake. Kulira kwawo kudzamveka mʼmazenera, mʼmakomo mwawo mudzakhala zinyalala zokhazokha, nsanamira za mkungudza zidzakhala poonekera.
15Umenewu ndiye mzinda wosasamala umene kale unali wotetezedwa. Unkanena kuti mu mtima mwake, “Ine ndine, ndipo palibenso wina wondiposa.” Taonani lero wasanduka bwinja, kokhala nyama zakutchire! Onse owudutsa akuwunyoza ndi kupukusa mitu yawo.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.