Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

ZEKARIYA 7

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Pa chaka chachinayi cha Mfumu Dariyo, pa tsiku lachinayi la Kisilevi, mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi Zekariya.
2Anthu a ku Beteli anali atatuma Sarezeri ndi Regemu-Meleki pamodzi ndi anthu awo, kuti akapemphe chifundo kwa Yehova
3pokafunsa kwa ansembe a ku Nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse ndi aneneri kuti, “Kodi ine ndizilira ndi kusala zakudya pa mwezi wachisanu, monga mmene ndakhala ndikuchitira pa zaka zambiri?”
4Pamenepo Yehova Wamphamvuzonse anayankhula nane kuti,
5“Funsa anthu onse a mʼdziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya pa mwezi wachisanu ndi wachisanu ndi chiwiri pa zaka 70 zapitazi, kodi munkasala chifukwa cha Ine?
6Ndipo pamene munkadya ndi kumwa, kodi simunkachita zimenezi podzisangalatsa nokha?
7Kodi awa si mawu amene Yehova ankanena kudzera mwa aneneri oyamba aja pamene Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira anali pa mtendere ndi pa ulemerero, ndi pamene Negevi ndi ku madera akumadzulo a mʼmbali mwa phiri munali anthu?’ ”
8Ndipo Yehova anayankhulanso ndi Zekariya kuti,
9“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni.
10Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’
11“Koma makolo anu anakana kumvera uthenga umenewu; anawumitsa mtima nandifulatira, natseka makutu awo kuti asamve.
12Anawumitsa mitima yawo ngati mwala wa sangalabwi ndipo sanamvere lamulo kapena mawu amene Yehova Wamphamvuzonse anawatumiza mwa Mzimu wake kudzera mwa aneneri oyamba aja. Kotero Yehova Wamphamvuzonse anakwiya kwambiri.
13“ ‘Pamene ndinawayitana, iwo sanamvere; choncho pamene iwo anandiyitana, Ine sindinamverenso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
14‘Ndinawamwaza ndi kamvuluvulu pakati pa mitundu yonse ya anthu, kumene anali alendo. Dziko lawo linatsala litasakazidwa kwambiri kotero kuti palibe amene amabwera kapena kupitamo. Umu ndi mmene anasandutsira dziko labwino kukhala chipululu.’ ”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.