Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

ZEKARIYA 4

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Kenaka mngelo amene amayankhula nane anabwerera nandidzutsa, ngati mmene amadzutsira munthu amene ali mʼtulo.
2Anandifunsa kuti, “Kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ine ndikuona choyikapo nyale, chonse chagolide ndi mbale pamwamba pake ndi nyale zoyaka zisanu ndi ziwiri, iliyonse ili ndi zibowo zisanu ndi ziwiri zolowetsera zingwe zoyatsira.
3Ndiponso pambali pake pali mitengo ya olivi iwiri, umodzi uli kumanja kwa mbaleyo ndipo winawo kumanzere.”
4Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi nʼchiyani mbuye wanga?”
5Iye anandiyankha kuti, “Kodi iwe sukuzidziwa zimenezi?” Ndinayankha kuti, “Ayi mbuye wanga.”
6Choncho iye anandiwuza kuti, “Mawu a Yehova kwa Zerubabeli ndi awa: ‘Osati mwa nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi Mzimu wanga,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.
7“Kodi ndiwe yani, iwe phiri lamphamvu? Pamaso pa Zerubabeli udzasanduka dziko losalala. Pamenepo adzabweretsa mwala wotsiriza. Akamadzawuyika pamwamba anthu adzafuwula kuti, ‘Mulungu adalitse Nyumbayi! Mulungu adalitse Nyumbayi!’ ”
8Ndipo Yehova anayankhulanso nane kuti,
9“Manja a Zerubabeli ndiwo ayika maziko a Nyumbayi; adzatsiriza ndi manja ake omwewo. Pamenepo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse ndiye anakutuma.
10“Ndani wanyoza tsiku la zinthu zazingʼono? Anthu adzasangalala akadzaona chingwe choyezera mʼmanja mwa Zerubabeli. (“Nyale zisanu ndi ziwirizi ndi maso a Yehova, amene amayangʼanayangʼana pa dziko lapansi.”)
11Kenaka ndinafunsa mngelo uja kuti, “Kodi mitengo ya olivi iwiri ili kumanja ndi kumanzere kwa choyikapo nyalechi ikutanthauza chiyani?”
12Ndinamufunsanso kuti, “Kodi nthambi ziwiri za mtengo wa olivi zomwe zili pambali pa mipopi yodzera mafuta iwiri yagolide zikutanthauza chiyani?”
13Iye anandiyankha kuti, “Kodi iwe sukuzidziwa zimenezi?” Ine ndinati, “Ayi mbuye wanga.”
14Choncho iye anati, “Amenewa ndi anthu awiri amene adzozedwa kuti atumikire Ambuye pa dziko lonse lapansi.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.