Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

ZEKARIYA 13

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1“Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.
2“Pa tsiku limenelo, ndidzafafaniziratu mayina a mafano mʼdziko, ndipo sadzawakumbukiranso,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndidzachotsa mʼdziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa.
3Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, ‘Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.’ Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya.
4“Pa tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha masomphenya ake. Sadzavala chovala chake chaubweya ndi cholinga chonamiza anthu.
5Iye adzati, ‘Sindine mneneri. Ndine mlimi; ndakhala ndi kulima munda kuyambira ubwana wanga.’
6Ngati wina adzamufunsa, ‘Zilonda zili mʼthupi lakoli ndi chiyani?’ Iye adzayankha kuti, ‘Zilondazi ndinazilandira mʼnyumba ya abwenzi anga.’
7“Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga, ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!” akutero Yehova Wamphamvuzonse. Kantha mʼbusa ndipo nkhosa zidzabalalika, ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono.
8Mʼdziko monse, akutero Yehova Wamphamvuzonse, “zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za anthu zidzakanthidwa ndi kuwonongeka; koma chigawo chimodzi chidzatsala mʼdzikomo.
9Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto; ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide. Adzayitana pa dzina langa ndipo Ine ndidzawayankha; Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’ ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’ ”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.