Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

TITO 1

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Ndine Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndinatumidwa kuti nditsogolere amene Mulungu anawasankha ku chikhulupiriro ndi ku chidziwitso cha choonadi chimene chimawafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu
2ndi kuwapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu amene sanama, analonjeza nthawi isanayambe.
3Pa nthawi yake Mulungu, Mpulumutsi wathu anawulula poyera mawu ake ndipo analamula kuti ndipatsidwe udindo wolalikira uthengawu.
4Kwa Tito, mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.
5Ndinakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene ndinazisiya zisanathe ndiponso usankhe akulu ampingo mʼmizinda yonse, monga momwe ndinakulamulira.
6Mkulu wampingo akhale munthu wopanda cholakwa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, munthu amene ana ake ndi okhulupirira, osati amakhalidwe oyipa ndi osamvera.
7Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo.
8Koma akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziretsa, wolungama, woyera mtima ndi wosunga mwambo.
9Iye ayenera kugwiritsa mawu okhulupirika monga tinaphunzitsira, kuti athe kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona ndiponso kugonjetsa amene atsutsana nacho.
10Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka mʼgulu la anthu a mdulidwe, oyankhula nkhani zopanda pake ndi kusocheretsa anzawo.
11Ayenera kuletsedwa kuyankhula chifukwa akusokoneza mabanja athunthu pophunzitsa zinthu zomwe sayenera kuwaphunzitsa. Iwo amachita izi kuti apeze ndalama mwachinyengo.
12Mneneri wina, mmodzi wa iwo omwewo anati, “Akrete nthawi zonse ndi amabodza, akhalidwe loyipitsitsa ndiponso alesi adyera.”
13Mawu amenewa ndi woona. Nʼchifukwa chake, uwadzudzule mwamphamvu, kuti akhale ndi chikhulupiriro choona,
14kuti asasamalenso nthano za Chiyuda, ndi malamulo a anthu amene akukana choonadi.
15Kwa oyera mtima, zinthu zonse ndi zoyera, koma kwa amene ndi odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera. Kunena zoona, mitima yawo ndi chikumbumtima chawo, zonse nʼzodetsedwa.
16Iwo amati amadziwa Mulungu, pamene ndi zochita zawo amamukana. Ndi anthu onyansa ndi osamvera, ndi osayenera kuchita kalikonse kabwino.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.