Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

NYIMBO YA SOLOMONI 3

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Usiku wonse ndili pa bedi langa ndinafunafuna amene mtima wanga umamukonda; ndinamufunafuna koma osamupeza.
2Ndikudzuka tsopano ndipo ndidzayendayenda mu mzinda, mʼmisewu yake ndi mʼmabwalo ake; ndidzamufunafuna amene mtima wanga umamukonda. Kotero ine ndinamufunafuna iyeyo koma osamupeza.
3Alonda anandipeza pamene ankayendera mzinda. “Kodi mwamuonako amene mtima wanga umamukonda?”
4Nditawapitirira pangʼono ndinamupeza amene mtima wanga umamukonda. Ndinamugwira ndipo sindinamulole kuti achoke mpaka nditamulowetsa mʼnyumba ya amayi anga, mʼchipinda cha amene anandibereka.
5Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo: Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho.
6Kodi ndani amene akubwera kuchokera ku chipululu ngati utsi watolotolo, wonunkhira mure ndi lubani, zopangidwa kuchokera ku zonunkhira zonse za anthu amalonda?
7Ona! Chimenecho ndi chonyamulira Solomoni, choperekezedwa ndi asilikali 60, anthu amphamvu a ku Israeli,
8onse atanyamula lupanga, onse odziwa bwino nkhondo, aliyense ali ndi lupanga pambali pake, kukonzekera zoopsa za usiku.
9Mfumu Solomoni anadzipangira chonyamulirachi; anachipanga ndi matabwa ochokera ku Lebanoni.
10Milongoti yake anayipanga yasiliva, kumbuyo kwake kwa golide. Mipando yake inakutidwa ndi nsalu yapepo, anakongoletsa mʼkati mwake ndi chikondi cha akazi a ku Yerusalemu.
11Tukulani inu akazi a ku Ziyoni ndipo mudzaone mfumu Solomoni atavala chipewa chaufumu, chipewa chaufumu chimene amayi ake anamuveka pa tsiku la ukwati wake, tsiku limene mtima wake unasangalala.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.