Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

NYIMBO YA SOLOMONI 1

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Nyimbo ya Solomoni, nyimbo yoposa nyimbo zonse.
2Undipsompsone ndi milomo yako chifukwa chikondi chako nʼchokoma kuposa vinyo.
3Mafuta ako odzola ndi onunkhira bwino; dzina lako lili ngati mafuta onunkhira otsanulidwa. Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda!
4Nditenge ndipo ndizikutsata, tiye tifulumire! Mfumu indilowetse mʼchipinda chake. Ife timasangalala ndi kukondwera nawe, tidzatamanda chikondi chako kupambana vinyo. Amachita bwinotu potamanda iwe!
5Ndine wakuda, komatu ndine wokongola, inu akazi a ku Yerusalemu, ine ndine wakuda ngati tenti ya ku Kedara, ngati makatani a tenti ya Solomoni.
6Musandiyangʼane monyoza chifukwa ndine wakuda, ndine wakuda chifukwa cha dzuwa. Alongo anga anandikwiyira ndipo anandigwiritsa ntchito mʼminda ya mpesa; munda wangawanga sindinawusamalire.
7Ndiwuze iwe, amene ndimakukonda, kumene umadyetsa ziweto zako ndi kumene umagoneka nkhosa zako nthawi yamasana. Ndikhalirenji ngati mkazi wachiwerewere pambali pa ziweto za abwenzi ako?
8Ngati sukudziwa iwe wokongola kwambiri kuposa akazi ena, ngati sukudziwa, tsatira makwalala a nkhosa ndipo udyetse ana ambuzi pambali pa matenti a abusa.
9Iwe bwenzi langa, uli ngati kavalo wamkazi ku magaleta a Farao.
10Masaya ako ndi okongola ndi ndolo zamʼmakutuzo, khosi lako likukongola ndi mikanda yamiyala yamtengowapatali.
11Tidzakupangira ndolo zagolide zokongoletsedwa ndi mikanda yasiliva.
12Pamene mfumu inali pa malo ake odyera, mafuta anga onunkhira anamveka fungo lake.
13Wokondedwa wanga ali ngati kathumba ka mure kwa ine, kamene kamakhala pakati pa mawere angawa.
14Wokondedwa wanga ali ngati mpukutu wa maluwa ofiira, ochokera ku minda ya mpesa ya ku Eni-Gedi.
15Iwe wokondedwa wanga, ndiwe wokongoladi! Ndithu, ndiwe chiphadzuwa, maso ako ali ngati nkhunda.
16Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongoladi! Ndithu, ndiwe wokongoladi kwambiri! Ndipo malo athu ogonapo ndi msipu wobiriwira.
17Mitanda ya nyumba yathu ndi ya mkungudza, phaso lake ndi la mtengo wa payini.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.