Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

AROMA 10

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe.
2Popeza ndiwachitira umboni kuti ndi achangu pa zinthu za Mulungu koma osati mwachidziwitso.
3Pakuti sanadziwe chilungamo chochokera kwa Mulungu ndipo anafuna kukhazikitsa chawochawo. Iwo sanagonjere chilungamo cha Mulungu.
4Khristu ndiye mathero amalamulo kuti aliyense amene akhulupirira akhale olungama pamaso pa Mulungu.
5Mose akulemba motere zachilungamo cha malamulo, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.”
6Koma chilungamo cha chikhulupiriro chikuti, “Usanene mu mtima mwako kuti, ‘Kodi ndani amene akwere kumwamba?’ ” (ndiko, kukatsitsa Khristu)
7“kapena ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’ ” (ndiko, kukamutenga Khristu kwa akufa).
8Nanga akuti chiyani? “Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu.” Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira,
9kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
10Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa.
11Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.”
12Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye
13pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”
14Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo?
15Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”
16Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?”
17Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.
18Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti, “Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi. Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”
19Ine ndifunsanso kuti, kodi Israeli sanazindikire? Poyamba Mose akuti, “Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake. Ine ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.”
20Ndipo Yesaya molimba mtima akuti, “Anandipeza anthu amene sanali kundifunafuna. Ndinadzionetsera kwa amene sanafunse za Ine.”
21Koma zokhudzana ndi Aisraeli akuti, “Tsiku lonse ndinatambasulira manja anga kwa anthu osandimvera ndi okanika.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.