Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 94

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango, Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.
2Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi; bwezerani kwa odzikuza zowayenera.
3Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova, mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?
4Amakhuthula mawu onyada; onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.
5Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova; amapondereza cholowa chanu.
6Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko; amapha ana amasiye.
7Iwo amati, “Yehova sakuona; Mulungu wa Yakobo salabadirako.”
8Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu; zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?
9Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva? Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?
10Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga? Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?
11Yehova amadziwa maganizo a munthu; Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.
12Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza, munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu;
13mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto, mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje.
14Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake; Iye sadzasiya cholowa chake.
15Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo, ndipo onse olungama mtima adzachitsata.
16Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa? Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?
17Yehova akanapanda kundithandiza, bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa.
18Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,” chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
19Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga, chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.
20Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake?
21Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe.
22Koma Yehova wakhala linga langa, ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako.
23Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo; Yehova Mulungu wathu adzawawononga.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.