Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 88

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa, usana ndi usiku ndimalira pamaso panu.
2Pemphero langa lifike pamaso panu; tcherani khutu lanu kuti mumve kulira kwanga.
3Pakuti ndili ndi mavuto ambiri ndipo moyo wanga ukuyandikira ku manda.
4Ndikuwerengedwa pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje; ndine munthu wopanda mphamvu.
5Ndayikidwa pambali pamodzi ndi anthu akufa, monga ophedwa amene agona mʼmanda, amene Inu simuwakumbukiranso, amene achotsedwa pa chisamaliro chanu.
6Mwandiyika pansi pa dzenje penipeni, mʼmalo akuya a mdima waukulu.
7Ukali wanu ukundipsinja kwambiri, mwandiopseza kwambiri ndi mafunde anu onse. Sela
8Mwandichotsa pakati pa abwenzi anga enieni ndipo mwachititsa kuti ndikhale chonyansa kwa iwo. Ndatsekerezedwa ndipo sindingathe kuthawa;
9maso anga ada ndi chisoni. Ndimayitana Inu Yehova tsiku lililonse; ndimakweza manja anga kwa Inu.
10Kodi mumaonetsa zozizwitsa zanu kwa anthu akufa? Kodi iwo amene afa amaukanso ndi kutamanda Inu? Sela
11Kodi chikondi chanu chimalalikidwa mʼmanda, za kukhulupirika kwanu ku malo a chiwonongeko?
12Kodi zozizwitsa zanu zimadziwika ku malo a mdima, kapena ntchito zanu zolungama ku dziko la anthu oyiwalika?
13Inu Yehova, Ine ndimalirira thandizo; mmawa mapemphero anga amafika pamaso panu.
14Inu Yehova nʼchifukwa chiyani mukundikana ndi kundibisira nkhope yanu?
15Kuyambira ubwana wanga ndakhala ndikuzunzika pafupi kufa; ndakhala ndikuchita mantha ndipo ndine wothedwa nzeru.
16Ukali wanu wandimiza; zoopsa zanu zandiwononga.
17Tsiku lonse zimandizungulira ngati chigumula; zandimiza kwathunthu.
18Inu mwatenga anzanga ndi okondedwa anga kuwachotsa pamaso panga; mdima ndiye bwenzi langa lenileni.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.