Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 7

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu; pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,
2mwina angandikadzule ngati mkango, ndi kundingʼamba popanda wondipulumutsa.
3Inu Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita izi ndipo ndapezeka wolakwa,
4ngati ndachita zoyipa kwa iye amene ndili naye pa mtendere, kapena popanda chifukwa ndalanda mdani wanga,
5pamenepo lolani adani anga andithamangitse ndi kundipitirira, lolani kuti moyo wanga aupondereze pansi ndipo mundigoneke pa fumbi. Sela
6Nyamukani Yehova, mu mkwiyo wanu; nyamukani kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga. Dzukani Mulungu wanga, lamulirani chilungamo chanu.
7Lolani gulu la anthu a mitundu ina lisonkhane mokuzungulirani. Alamulireni muli kumwambako;
8Yehova aweruzeni anthu a mitundu inayo. Ndiweruzeni Yehova, monga mwa chilungamo changa, monga mwa moyo wanga wangwiro, Inu Wammwambamwamba.
9Inu Mulungu wolungama, amene mumasanthula maganizo ndi mitima, thetsani chiwawa cha anthu oyipa ndipo wolungama akhale motetezedwa.
10Chishango changa ndi Mulungu Wammwambamwamba, amene amapulumutsa olungama mtima.
11Mulungu amaweruza molungama, Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.
12Ngati munthu satembenuka, Mulungu adzanola lupanga lake, Iye adzawerama ndi kukoka uta.
13Mulungu wakonza zida zake zoopsa; Iye wakonzekera mivi yake yoyaka moto.
14Taonani, munthu woyipa amalingalira zoyipa zokhazokha nthawi zonse. Zochita zake ndi zosokoneza ndi zovutitsa anthu ena.
15Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsa amagwera mʼdzenje limene wakumbalo.
16Mavuto amene amayambitsa amamubwerera mwini; chiwawa chake chimatsikira pa mutu wake womwe.
17Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake; ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.