Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 41

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.
2Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake.
3Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.
4Ndinati, “Inu Yehova, mundichitire chifundo; chiritseni pakuti ndakuchimwirani.”
5Adani anga mwankhwidzi amanena za ine kuti, “Kodi munthu ameneyu adzafa liti kuti ayiwalike?”
6Pamene wina abwera kudzandiona, amayankhula mwachinyengo, pomwe mtima wake ukusonkhanitsa zachipongwe; kenaka iye amatuluka ndi kukalengeza kunja.
7Adani anga onse amanongʼonezana pamodzi kulimbana nane, iwo amalingalira zoyipa kwambiri za ine, ponena kuti,
8“Matenda owopsa amugwira; sadzaukapo pamalo pamene wagona.”
9Ngakhale bwenzi langa la pamtima amene ndinamudalira, iye amene amadya pamodzi ndi ine watukula chidendene chake kulimbana nane.
10Koma Yehova mundichititre chifundo, dzutseni kuti ndiwabwezere.
11Ine ndikudziwa kuti mukukondwera nane, pakuti mdani wanga sandigonjetsa.
12Mu ungwiro wanga Inu mumandisunga ndi kundiyimika pamaso panu kwamuyaya.
13Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli kuchokera muyaya mpaka muyaya. Ameni ndi Ameni.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.