Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 33

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama, nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.
2Mutamandeni Yehova ndi pangwe; muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.
3Muyimbireni nyimbo yatsopano; imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.
4Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona; Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita.
5Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama; dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.
6Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa, zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
7Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko; amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.
8Dziko lonse lapansi liope Yehova; anthu onse amulemekeze Iye.
9Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo; Iye analamulira ndipo zinakhazikika.
10Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina; Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.
11Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya, zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.
12Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova, anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
13Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi ndi kuona anthu onse;
14kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira onse amene amakhala pa dziko lapansi.
15Iye amene amapanga mitima ya onse, amaona zonse zimene akuchita.
16Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo; palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.
17Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso, ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.
18Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye; amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,
19kuwawombola iwo ku imfa ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.
20Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo; Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.
21Mwa Iye mitima yathu imakondwera, pakuti ife timadalira dzina lake loyera.
22Chikondi chanu chosatha chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.