Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 29

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
2Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake, pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.
3Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi; Mulungu waulemerero abangula, Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
4Liwu la Yehova ndi lamphamvu; liwu la Yehova ndi laulemerero.
5Liwu la Yehova limathyola mikungudza; Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
6Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe, Siriyoni ngati mwana wa njati:
7Liwu la Yehova limakantha ngati kungʼanima kwa mphenzi.
8Liwu la Yehova limagwedeza chipululu; Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
9Liwu la Yehova limapindapinda mibawa ndi kuyeretsa nkhalango. Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”
10Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira, Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
11Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake; Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.