Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 24

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo, dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;
2pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja ndi kulikhazika pamwamba pa madzi.
3Ndani angakwere phiri la Yehova? Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?
4Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera, amene sapereka moyo wake kwa fano kapena kulumbira mwachinyengo.
5Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
6Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova; amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo. Sela
7Tukulani mitu yanu inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
8Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.
9Tukulani mitu yanu, inu zipata; tsekukani, inu zitseko zakalekalenu, kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
10Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Yehova Wamphamvuzonse, Iye ndiye Mfumu yaulemerero. Sela
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.