Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 135

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Tamandani Yehova. Tamandani dzina la Yehova; mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
2amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova, mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.
3Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino; imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero,
4Pakuti Yehova wasankha Yakobo kuti akhale wake, Israeli kuti akhale chuma chake chapamtima.
5Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu, kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.
6Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera, kumwamba ndi dziko lapansi, ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.
7Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvula ndipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.
8Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto, ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.
9Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto, kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.
10Iye anakantha mitundu yambiri ya anthu ndi kupha mafumu amphamvu:
11Sihoni mfumu ya Aamori, Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a ku Kanaani;
12ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa, cholowa cha anthu ake Aisraeli.
13Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya, mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.
14Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa, ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.
15Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu.
16Pakamwa ali napo koma sayankhula maso ali nawo, koma sapenya;
17makutu ali nawo, koma sakumva ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse.
18Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo, chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.
19Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova; inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova;
20Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova; Inu amene mumaopa Iye, tamandani Yehova.
21Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni, amene amakhala mu Yerusalemu. Tamandani Yehova.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.