Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 115

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi koma ulemerero ukhale pa dzina lanu, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
2Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti, “Mulungu wawo ali kuti?”
3Mulungu wathu ali kumwamba; Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
4Koma mafano awo ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu.
5Pakamwa ali napo koma sayankhula, maso ali nawo koma sapenya;
6makutu ali nawo koma samva, mphuno ali nazo koma sanunkhiza;
7manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu; mapazi ali nawo koma sayenda; kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.
8Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo, chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
9Inu Aisraeli, dalirani Yehova; Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
10Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova; Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.
11Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova; Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
12Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa: adzadalitsa nyumba ya Israeli, adzadalitsa nyumba ya Aaroni,
13adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova; aangʼono ndi aakulu omwe.
14Yehova akuwonjezereni madalitso; inuyo pamodzi ndi ana anu.
15Mudalitsidwe ndi Yehova, Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16Kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
17Si anthu akufa amene amatamanda Yehova, amene amatsikira kuli chete;
18ndi ife amene timatamanda Yehova, kuyambira tsopano mpaka muyaya. Tamandani Yehova.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.