Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MASALIMO 10

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Nʼchifukwa chiyani Yehova mwayima patali? Chifukwa chiyani mukudzibisa nokha pa nthawi ya mavuto?
2Mwa kunyada kwake munthu woyipa asaka wofowoka, amene akodwa mʼnjira zimene iye wakonza.
3Iye amatamandira zokhumba za mu mtima wake; amadalitsa aumbombo ndi kuchitira chipongwe Yehova.
4Mwa kunyada kwake woyipa safunafuna Mulungu; mʼmaganizo ake wonse mulibe malo a Mulungu.
5Zinthu zake zimamuyendera bwino; iye ndi wamwano ndipo malamulo anu ali nawo kutali; amanyogodola adani ake onse.
6Iye amadziyankhulira kuti, “Palibe chimene chidzandigwedeze. Ndidzakhala wokondwa nthawi zonse ndipo sindidzakhala pa mavuto.”
7Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi zoopseza; zovutitsa ndi zoyipa zili pansi pa lilime lake.
8Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi, kuchokera pobisalapo amapha anthu osalakwa, amayangʼanayangʼana mwachinsinsi anthu oti awawononge.
9Amabisalira anthu ngati mkango pa zitsamba. Amabisalira kuti agwire anthu opanda mphamvu; amagwira anthu opanda mphamvu ndi kuwakokera mu ukonde wake.
10Anthuwo amawapondaponda ndipo amakomoka; amakhala pansi pa mphamvu zake.
11Iye amati mu mtima mwake, “Mulungu wayiwala, wabisa nkhope yake ndipo sakuonanso.”
12Dzukani Yehova! Onetsani dzanja lanu Inu Mulungu. Musayiwale anthu opanda mphamvu.
13Nʼchifukwa chiyani munthu woyipa amachitira chipongwe Mulungu? Chifukwa chiyani amati mu mtima mwake, “Iye sandiyimba mlandu?”
14Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa, mumaganizira zochitapo kanthu. Wovutikayo amadzipereka yekha kwa Inu pakuti Inu ndi mthandizi wa ana amasiye.
15Thyolani dzanja la woyipitsitsa ndi la munthu woyipa; muzengeni mlandu chifukwa cha zoyipa zake zimene sizikanadziwika.
16Yehova ndi Mfumu kwamuyaya; mitundu ya anthu idzawonongeka kuchoka mʼdziko lake.
17Mumamva Inu Yehova, zokhumba za osautsidwa; mumawalimbikitsa ndipo mumamva kulira kwawo.
18Kuteteza ana amasiye ndi oponderezedwa, ndi cholinga chakuti munthu amene ali wa dziko lapansi asaopsenso.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.