Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MIYAMBO 7

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Mwana wanga, mvera mawu anga; usunge bwino malamulo angawa.
2Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo; samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako.
3Uchite ngati wawamangirira pa zala zako, ndiponso ngati kuti wawalemba pa mtima pako.
4Nzeru uyiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,” ndipo khalidwe lomvetsa bwino zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.”
5Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololo ndiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo.
6Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga ndinasuzumira pa zenera.
7Ndinaona pakati pa anthu opusa, pakati pa anyamata, mnyamata wina wopanda nzeru.
8Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo, kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo.
9Inali nthawi yachisisira madzulo, nthawi ya usiku, kuli mdima.
10Ndipo mkaziyo anadzakumana naye, atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga.
11(Mkaziyo ndi wolongolola ndiponso nkhutukumve, iye ndi wosakhazikika pa khomo.
12Mwina umupeza pa msewu, mwina umupeza pa msika, ndipo amadikirira munthu pa mphambano iliyonse).
13Tsono amagwira mnyamatayo ndi kupsompsona ndi nkhope yake yopanda manyazi amamuwuza kuti,
14“Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano. Lero ndakwaniritsa malumbiro anga.
15Choncho ndinabwera kudzakumana nawe; ndinkakufunafuna ndipo ndakupeza!
16Pa bedi panga ndayalapo nsalu zosalala zokongola zochokera ku Igupto.
17Pa bedi panga ndawazapo zonunkhira za mure, mafuta onunkhira a aloe ndi sinamoni.
18Bwera, tiye tikhale malo amodzi kukondwerera chikondi mpaka mmawa; tiye tisangalatsane mwachikondi!
19Mwamuna wanga kulibe ku nyumbako; wapita ulendo wautali:
20Anatenga thumba la ndalama ndipo adzabwera ku nyumba mwezi ukakhwima.”
21Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo; amukopa ndi mawu ake oshashalika.
22Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo ngati ngʼombe yopita kukaphedwa, monga momwe mbawala ikodwera mu msampha,
23mpaka muvi utalasa chiwindi chake, chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe, osadziwa kuti moyo wake uwonongeka.
24Tsono ana inu, ndimvereni; mvetsetsani zimene ndikunena.
25Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu; musasochere potsata njira zake.
26Paja iye anagwetsa anthu ambiri; wapha gulu lalikulu la anthu.
27Nyumba yake ndi njira yopita ku manda, yotsikira ku malo a anthu akufa.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.