Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

NEHEMIYA 1

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Awa ndi mawu a Nehemiya mwana wa Hakaliya: Pa mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pamene ndinali mu mzinda wa Susa,
2Hanani mmodzi mwa abale anga, anabwera ndi anthu ena kuchokera ku Yuda, ndipo ine ndinawafunsa za Ayuda otsala amene sanatengedwe ukapolo, ndiponso za mzinda wa Yerusalemu.
3Anandiyankha kuti, “Amene sanatengedwe ukapolo aja ali pa mavuto aakulu ndipo ali ndi manyazi. Khoma la Yerusalemu ndilogamukagamuka ndipo zipata zake zinatenthedwa ndi moto.”
4Nditamva zimenezi, ndinakhala pansi ndi kuyamba kulira. Ndinalira kwa masiku angapo. Ndinkasala zakudya ndi kumapemphera pamaso pa Mulungu Wakumwamba.
5Ndinkati: “Inu Yehova, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa. Mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu.
6Tcherani khutu lanu ndi kutsekula maso anu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune limene ndikupemphera usana ndi usiku pamaso panu kupempherera Aisraeli, atumiki anu. Ndikuvomereza machimo a Aisraeli amene tinakuchimwirani. Ndithu, ine ndi banja la makolo anga tinakuchimwirani.
7Ife tinakuchitirani zoyipa zambiri. Sitinamvere mawu anu, malamulo ndi malangizo anu amene munapereka kwa mtumiki wanu Mose.
8“Kumbukirani mawu amene munawuza mtumiki wanu Mose akuti, ‘Ngati mukhala osakhulupirika, ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina.
9Koma mukabwerera kwa Ine, mukamvera malamulo anga ndi kuwatsatadi, ndiye kuti ngakhale anthu anu atabalalika kutali chotani, Ine ndidzawasonkhanitsa kuchokera kumeneko ndi kubwera nawo ku malo amene ndinasankha kuti azidzayitanira dzina langa.’
10“Iwo ndi atumiki anu ndi anthu anu, amene munawawombola ndi mphamvu yanu yayikulu ndi dzanja lanu lamphamvu.
11Inu Ambuye tcherani khutu lanu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu amene amakondwera kuchitira ulemu dzina lanu. Lolani kuti mtumiki wanune zinthu zindiyendere bwino lero ndi kuti mfumu indichitire chifundo.” Nthawi imeneyi nʼkuti ndili woperekera zakumwa kwa mfumu.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.