Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MIKA 2

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Tsoka kwa amene amakonzekera chiwembu, kwa amene amakonzekera kuchita zoyipa usiku pa mabedi awo! Kukacha mmawa amakachitadi chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.
2Amasirira minda ndi kuyilanda, amasirira nyumba ndi kuzilanda. Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo, munthu mnzawo kumulanda cholowa chake.
3Nʼchifukwa chake Yehova akuti, “Ine ndikukonzekera kubweretsa tsoka pa anthu awa, tsoka limene simudzatha kudzipulumutsa nokha. Inu simudzayendanso monyada, pakuti idzakhala nthawi ya masautso.
4Tsiku limenelo anthu adzakuchitani chipongwe; adzakunyogodolani ndi nyimbo iyi yamaliro: ‘Tawonongeka kotheratu; dziko la anthu anga lagawidwa. Iye wandilanda! Wapereka minda yathu kwa anthu otiwukira.’ ”
5Nʼchifukwa chake simudzakhala ndi munthu mu msonkhano wa Yehova kuti agawe dziko pochita maere.
6Aneneri awo amanena kuti, “Usanenere! Usanenere ndi pangʼono pomwe zimenezi; ife sitidzachititsidwa manyazi.”
7Inu nyumba ya Yakobo, monga zimenezi ndi zoyenera kuzinena: “Kodi Mzimu wa Yehova wakwiya? Kodi Iye amachita zinthu zotere?” “Kodi mawu ake sabweretsa zabwino kwa amene amayenda molungama?
8Posachedwapa anthu anga andiwukira ngati mdani. Mumawavula mkanjo wamtengowapatali anthu amene amadutsa mosaopa kanthu, monga anthu amene akubwera ku nkhondo.
9Mumatulutsa akazi a anthu anga mʼnyumba zawo zabwino. Mumalanda ana awo madalitso anga kosatha.
10Nyamukani, chokani! Pakuti ano si malo anu opumulirapo, chifukwa ayipitsidwa, awonongedwa, sangatheke kuwakonzanso.
11Ngati munthu wabodza ndi wachinyengo abwera nʼkunena kuti, ‘Ine ndidzanenera ndipo mudzakhala ndi vinyo ndi mowa wambiri, woteroyo adzakhala mneneri amene anthu awa angamukonde!’
12“Inu banja la Yakobo, ndidzakusonkhanitsani nonse; ndidzawasonkhanitsa pamodzi otsala a ku Israeli. Ndidzawabweretsa pamodzi ngati nkhosa mʼkhola, ngati ziweto pa msipu wake; malowo adzadzaza ndi chinamtindi cha anthu.
13Amene adzawapulumutse adzayenda patsogolo pawo; iwo adzathyola chipata ndipo adzatuluka. Mfumu yawo idzawatsogolera, Yehova adzakhala patsogolo pawo.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.