Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MATEYU 28

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Litapita tsiku la Sabata, mmawa wa tsiku loyamba la Sabata, Mariya wa ku Magadala ndi Mariya wina anapita kukaona manda.
2Kunachitika chivomerezi chachikulu, pakuti mngelo wa Ambuye anabwera kuchokera kumwamba ndipo anapita ku manda, nakagubuduza mwala nawukhalira.
3Maonekedwe ake anali ngati mphenzi ndipo zovala zake zinali mbuu ngati matalala.
4Alondawo anachita naye mantha kwambiri kotero kuti ananjenjemera ndi kuwuma ngati akufa.
5Mngelo anati kwa amayiwo, “Musachite mantha popeza ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anapachikidwa.
6Iye muno mulibe, wauka monga mmene ananenera. Bwerani, dzaoneni malo amene anagona.
7Ndipo pitani msanga kawuzeni ophunzira ake kuti, ‘Wauka kwa akufa ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona Iye kumeneko.’ Taonani ndakuwuzani.”
8Pamenepo amayiwo anachoka mofulumira ku mandako ali ndi mantha komabe atadzaza ndi chimwemwe, ndipo anathamanga kukawuza ophunzira ake.
9Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo nati, “Moni.” Iwo anabwera kwa Iye, nagwira mapazi ake namulambira.
10Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Musachite mantha, pitani kawuzeni abale anga kuti apite ku Galileya ndipo kumeneko akandiona Ine.”
11Amayi aja akupita, ena mwa alonda aja anapita ku mzinda nafotokozera akulu a ansembe zonse zimene zinachitika.
12Akulu a ansembe atakumana ndi akuluakulu anapangana zochita. Anapatsa alonda aja ndalama zambiri,
13nawawuza kuti, “Muzinena kuti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku ndipo amuba ife tili mtulo.’
14Ngati nkhani iyi imupeze bwanamkubwa, ife tidzamukhazika mtima pansi ndipo simudzakhala mʼmavuto.”
15Pamenepo alondawo anatenga ndalamazo nachita monga mmene anawuzidwira. Ndipo mbiri iyi inawanda pakati pa Ayuda mpaka lero lino.
16Ndipo ophunzira khumi ndi mmodzi aja anapita ku Galileya, ku phiri limene Yesu anawawuza kuti apite.
17Atamuona Iye, anamulambira; koma ena anakayika.
18Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine.
19Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera,
20ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.