Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YOSWA 23

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Panapita nthawi yayitali kuchokera pamene Yehova anakhazikitsa mtendere pakati pa Aisraeli ndi adani awo owazungulira. Nthawi imeneyi nʼkuti Yoswa atakalamba, ali ndi zaka zambiri.
2Yoswayo anayitanitsa Aisraeli onse pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, oweruza, ndi oyangʼanira anthu antchito ndipo anawawuza kuti, “Ine ndakalamba ndipo ndili ndi zaka zambiri.
3Inu mwaona zonse zimene Yehova Mulungu wanu wachita kwa mitundu yonseyi chifukwa cha inu. Ndi Yehova Mulungu wanu amene anakumenyerani nkhondo.
4Tsono onani! Mitundu ya anthu otsalawa ndayipereka kwa mafuko anu pamodzi ndi mitundu ya anthu ya pakati pa Yorodani ndi Nyanja Yayikulu ya kumadzulo imene ndinayigonjetsa.
5Yehova Mulungu wanu ndiye adzawathamangitsa pamaso panu. Mudzatenga dziko lawo monga Yehova anakulonjezerani.
6“Choncho khalani amphamvu, ndipo samalani kuti mumvere zonse zimene zalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose. Musapatuke pa malamulo onse amene alembedwamo.
7Musagwirizane ndi mitundu ya anthu imene yatsala pakati panu. Musatchule mayina a milungu yawo kapena kuyitchula polumbira. Musayitumikire kapena kuyigwadira.
8Koma mukuyenera kugwiritsa Yehova Mulungu wanu, monga mwachitira mpaka lero lino.
9“Yehova wapirikitsa patsogolo panu mitundu ya anthu ikuluikulu ndi yolimba. Mpaka lero palibe amene watha kulimbana nanu.
10Aliyense wa inu atha kuthamangitsa anthu 1,000 chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye amakumenyerani nkhondo, monga momwe analonjezera.
11Choncho samalitsani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.
12“Koma ngati mubwerera mʼmbuyo ndi kuphatikizana ndi mitundu yotsalayi imene ili pakati panu ndi kumakwatirana nayo,
13pamenepo mudziwe kuti Yehova, Mulungu wanu, sadzapirikitsa mitundu imeneyi pamaso panu, koma idzakhala ngati msampha kwa inu kapenanso khwekhwe lokukolani. Idzakhala ngati zikwapu pa msana panu kapenanso ngati minga mʼmaso mwanu mpaka mutatha psiti mʼdziko labwinoli limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.
14“Aliyense wa inu akudziwa mu mtima mwake komanso mʼmoyo mwake kuti zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wanu anakulonjezani zachitika. Palibe lonjezo ndi limodzi lomwe limene silinakwaniritsidwe.
15Monga momwe Yehova Mulungu wanu wakuchitirani zabwino zonse zimene ananena kuti adzachita, Yehovayo angathenso kukuchitirani zoyipa zonse zimene waopseza, mpaka kukuchotsani mʼdziko lokoma limene anakupatsani.
16Ngati muphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu, limene anakulamulirani nʼkumapita kukatumikira milungu ina ndi kuyigwadira, Yehova adzakukwiyirani, ndiye mudzachotsedwa mʼdziko labwinoli limene Yehova wakupatsani.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.