Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YOBU 8

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,
2“Kodi udzakhala ukuyankhula zoterezi mpaka liti? Mawu ako ali ngati mphepo yamkuntho.
3Kodi Mulungu amapotoza chiweruzo cholungama? Kodi Wamphamvuzonse amalephera kuchita zachilungamo?
4Pamene ana ako anamuchimwira Mulungu, Iye anawapereka kuti alangidwe chifukwa cha tchimo lawo.
5Koma utayangʼana kwa Mulungu, ndi kudandaulira Wamphamvuzonse,
6ngati uli wangwiro ndi wolungama mtima ngakhale tsopano Iye adzachitapo kanthu mʼmalo mwako ndipo adzakubwezeretsa pa malo ako oyenera.
7Chiyambi chako chidzaoneka ngati chochepa koma chimaliziro chako chidzakhala chopambana.
8“Funsa kwa anthu amvulazakale ndipo upeze zimene makolo awo anaziphunzira
9pakuti ife ndife ana adzulodzuloli ndipo sitidziwa chilichonse, ndipo moyo wathu pa dziko lapansi uli ngati chithunzithunzi.
10Kodi iwo sadzakulangiza ndi kukufotokozera? Kodi sadzakuwuza mawu ochokera pa zimene amazidziwa?
11Kodi bango nʼkumera pa nthaka yopanda chinyontho? Nanga mawango nʼkukula bwino popanda madzi?
12Popanda madzi, zimenezi zimafota zikanali zaziwisi ndi zosadula; zimawuma msangamsanga kuposa bango.
13Ndimo mmene amachitira anthu onse amene amayiwala Mulungu; ndi mmene chiyembekezo cha munthu wosapembedza Mulungu chimathera.
14Kulimba mtima kwake kumafowoka; zimene iye amadalira zili ngati ukonde wa kangawude.
15Iye amatsamira ukonde wake, koma umaduka; amawugwiritsitsa koma sulimba.
16Munthu woyipayo ali ngati chomera chothiriridwa bwino chimene chili pa dzuwa, nthambi zake zimatambalala pa munda wake;
17mizu yake imayanga pa mulu wa miyala ndi kufunafuna malo woti izikike pa miyalapo.
18Koma pamene yachotsedwa pamalo pakepo, pamalopo pamakana chomeracho ndi kuti, ‘Ine sindinakuonepo.’
19Ndithudi chomeracho chimafota, ndipo pa nthakapo pamatuluka zomera zina.
20“Ndithudi, Mulungu sakana munthu amene alibe cholakwa kapena kulimbikitsa anthu ochita zoyipa.
21Iye adzadzaza mʼkamwa mwako ndi phwete ndipo milomo yako idzafuwula ndi chimwemwe.
22Adani ako adzachita manyazi, ndipo malo okhalamo anthu oyipa sadzaonekanso.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.