Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YOBU 18

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,
2“Kodi iwe Yobu utsiriza liti zoyankhula zakozi? Khala munthu wozindikira zinthu ndipo ukatero ife tidzayankhula.
3Chifukwa chiyani ukutiyesa ngati ngʼombe ndi kuoneka ngati opusa mʼmaso mwako?
4Iwe amene ukudzipweteka wekha ndi mkwiyo wako, kodi dziko lapansi lisanduke bwinja chifukwa cha iweyo? Kodi kapena thanthwe lisunthidwe kuchoka pa malo ake?
5“Nyale ya munthu woyipa yazimitsidwa; malawi a moto wake sakuwalanso.
6Kuwala kwa mʼnyumba mwake kwasanduka mdima; nyale ya pambali pake yazima.
7Mayendedwe ake amgugu azilala; fundo zake zomwe zamugwetsa.
8Mapazi ake amulowetsa mu ukonde ndipo akungoyendayenda mu ukondewo.
9Msampha wamkola mwendo; khwekhwe lamugwiritsitsa.
10Amutchera msampha pansi mobisika; atchera diwa pa njira yake.
11Zoopsa zikumuchititsa mantha kumbali zonse, zikutsatira mayendedwe ake onse.
12Mphamvu zake zatha chifukwa cha njala, tsoka likumudikira.
13Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse; miyendo yake, manja ake, zonse zawola.
14Wachotsedwa mʼnyumba imene ankadalira, ndipo amukokera ku imfa, mfumu ya zoopsa zonse.
15Mʼnyumba mwake zonse zachotsedwamo; awazamo sulufule kuti aphe tizirombo ta matenda.
16Mizu yake ikuwuma pansi ndipo nthambi zake zikufota
17Sadzakumbukiridwanso pa dziko lapansi; sadzakhalanso ndi chinthu chomutchukitsa mʼdziko.
18Amuchotsa pa malo owala ndi kumuponya ku mdima, ndipo amupirikitsa pa dziko lonse.
19Iye alibe ana kapena zidzukulu pakati pa anthu ake, kulibe wotsala kumene iye ankakhala.
20Anthu akumadzulo adabwa kwambiri ndi tsoka lake; anthu akummawa agwidwa ndi mantha aakulu.
21Ndithudi, izi ndiye zimagwera munthu woyipa; amenewa ndiye mathero a munthu amene sadziwa Mulungu.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.