Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YOBU 16

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2“Ndinamvapo zambiri monga zimenezi; nonsenu ndinu anthu osatha kutonthoza mtima mnzanu.
3Kodi mawu anu ochulukawo adzatha? Kodi chikukuvutani nʼchiyani kuti muzingoyankhula mawu otsutsawa?
4Inenso ndikanatha kuyankhula monga inu, inuyo mukanakhala monga ndilili inemu; Ine ndikanatha kuyankhula mawu omveka bwino kutsutsana nanu ndi kukupukusirani mutu wanga.
5Ndipo mawu a pakamwa panga akanakulimbikitsani; chitonthozo chochokera pa milomo yanga chikanachepetsa ululu wanu.
6“Koma ine ndikati ndiyankhule ululu wanga sukuchepa; ndipo ndikati ndikhale chete, ululu wanga sukuchokabe.
7Ndithudi, Inu Mulungu mwanditha mphamvu; mwawononga banja langa lonse.
8Inu mwandimanga ndipo kundimangako kwakhala umboni; kuwonda kwanga kwandiwukira ndipo kukuchita umboni wonditsutsa.
9Mulungu amabwera kwa ine mwankhanza ndipo amadana nane, amachita kulumira mano; mdani wanga amandituzulira maso.
10Anthu amatsekula pakamwa pawo kundikuwiza; amandimenya pa tsaya mwachipongwe ndipo amagwirizana polimbana nane.
11Mulungu wandipereka kwa anthu ochita zoyipa ndipo wandiponyera mʼmanja mwa anthu oyipa mtima.
12Ine ndinali pamtendere, koma Mulungu ananditswanya; anandigwira pa khosi ndi kundiphwanya. Iye anandisandutsa choponyera chandamale chake;
13anthu ake oponya mauta andizungulira. Mopanda kundimvera chisoni, Iye akulasa impsyo zanga ndipo akutayira pansi ndulu yanga.
14Akundivulaza kawirikawiri, akuthamangira pa ine monga munthu wankhondo.
15“Ndasokerera chiguduli pa thupi langa ndipo ndayika mphamvu zanga pa fumbi.
16Maso anga afiira ndi kulira, ndipo zikope zanga zatupa;
17komatu manja anga sanachite zachiwawa ndipo pemphero langa ndi lolungama.
18“Iwe dziko lapansi, usakwirire magazi anga; kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke!
19Ngakhale tsopano mboni yanga ili kumwamba; wonditchinjiriza pa mlandu wanga ali komweko.
20Wondipembedzera ndi bwenzi langa, pamene maso anga akukhuthula misozi kwa Mulungu;
21iye, mʼmalo mwanga, amamudandaulira Mulungu monga munthu amadandaulira bwenzi lake.
22“Pakuti sipapita zaka zambiri ndisanayende mʼnjira imene sindidzabwerera.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.