Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YEREMIYA 20

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Wansembe Pasuri mwana wa Imeri, woyangʼanira wamkulu wa Nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya akulosera zinthu zimenezi.
2Tsono iye analamula kuti mneneri Yeremiyayo amenyedwe ndi kuyikidwa mʼndende pa Chipata chakumtunda kwa Benjamini ku Nyumba ya Yehova.
3Mmawa mwake, Pasuri anatulutsa Yeremiya mʼndende, ndipo Yeremiyayo anamuwuza kuti, “Pasuri, Yehova sadzakutchulanso dzina lako kuti Pasuri koma Zoopsa pa Mbali Zonse.
4Pakuti Yehova akuti, ‘Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe ndi kwa abwenzi ako onse; iweyo ukuona. Anthu a ku Yuda ndidzawapereka onse mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ena adzatengedwa ukapolo ku Babuloni ndipo ena adzaphedwa pa nkhondo.
5Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni.
6Ndipo iwe, Pasuri, pamodzi ndi onse a pa banja pako mudzapita ku ukapolo ku Babuloni. Mudzafera kumeneko ndi kuyikidwa mʼmanda, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unawalosera zabodza.’ ”
7Inu Yehova, mwandinamiza, ndipo ndinapusadi; Inu ndi wamphamvu kuposa ine ndipo munandipambana. Anthu akundinyoza tsiku lonse. Aliyense akundiseka kosalekeza.
8Nthawi iliyonse ndikamayankhula, ndimafuwula kunena kuti, ziwawa kuno! Tikuwonongeka! Mawu anu Yehova andisandutsa chinthu chonyozeka ndipo ndimachitidwa chipongwe tsiku lonse.
9Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iye kapena kuyankhulanso mʼdzina lake,” mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga, amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga. Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa, koma sindingathe kupirirabe.
10Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti, “Zoopsa ku mbali zonse! Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!” Onse amene anali abwenzi anga akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti, “Mwina mwake adzanyengedwa; tidzamugwira ndi kulipsira pa iye.”
11Koma Yehova ali nane, ndiye wankhondo wamphamvu. Nʼchifukwa chake ondizunza adzalephera ndipo sadzandipambana. Adzachita manyazi kwambiri chifukwa sadzapambana. Manyazi awo sadzayiwalika konse.
12Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumayesa anthu molungama ndipo mupenya za mu mtima mwa munthu. Ndiloleni kuti ndione kuti mwalipsira adani anga popeza ndapereka mlandu wanga kwa Inu.
13Imbirani Yehova! Mutamandeni Yehova! Iye amapulumutsa wosauka mʼmanja mwa anthu oyipa.
14Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa! Tsiku limene amayi anga anandibereka lisatamandidwe!
15Wotembereredwa munthu amene anapita kukasangalatsa abambo anga ndi uthenga woti: “Kwabadwa mwana wamwamuna!”
16Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene Yehova anayiwononga mopanda chisoni. Amve mfuwu mmawa, phokoso la nkhondo masana.
17Chifukwa sanandiphere mʼmimba, kuti amayi anga asanduke manda anga, mimba yawo ikhale yayikulu mpaka kalekale.
18Kodi ndinabadwira mavuto ndi chisoni kuti moyo wanga ukhale wamanyazi wokhawokha?
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.