Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YEREMIYA 12

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Yehova, Inu mumakhala wokhoza nthawi zonse ndikati nditsutsane nanu. Komabe ndikufuna kuyankhula nanu za mlandu wanga. Chifukwa chiyani anthu oyipa zinthu zimawayendera bwino? Chifukwa chiyani anthu achinyengo amakhala pabwino?
2Inu munawadzala ndipo anamera mizu; amakula ndi kubereka zipatso. Dzina lanu limakhala pakamwa pawo nthawi zonse, koma mitima yawo imakhala kutali ndi Inu.
3Koma Inu Yehova, ine mumandidziwa; mumandiona ndipo mumayesa zolingalira zanga. Akokeni anthu oyipawo ngati nkhosa zokaphedwa! Ayikeni padera mpaka tsiku loti akaphedwe!
4Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti ndipo udzu mʼmunda uliwonse udzakhalabe ofota mpaka liti? Nyama ndi mbalame kulibiretu chifukwa anthu amene amakhalamo ndi oyipa. Iwo amati: “Yehova sangathe kuona ntchito zathu.”
5Yehova anayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga pamodzi ndi anthu nanga ungapikisane bwanji ndi akavalo? Ngati ukupunthwa ndi kugwa pa malo abwino, udzatha bwanji kuthamanga mʼnkhalango za ku Yorodani?
6Ngakhale abale ako ndi anansi akuwukira, onsewo amvana zokuyimba mlandu. Usawakhulupirire, ngakhale ayankhule zabwino ndi iwe.
7“Ine ndawasiya anthu anga; anthu amene ndinawasankha ndawataya. Ndapereka okondedwa anga mʼmanja mwa adani awo.
8Anthu amene ndinawasankha asanduka ngati mkango wa mʼnkhalango. Akundibangulira mwaukali; nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawo.
9Anthu anga amene ndinawasankha asanduka ngati mbalame yolusa yamawangamawanga imene akabawi ayizinga. Pitani, kasonkhanitseni nyama zakuthengo. Mubwere nazo kuti zidzadye mbalameyo.
10Abusa ambiri anawononga munda wanga wa mpesa, anapondereza munda wanga; munda wanga wabwino uja anawusandutsa chipululu.
11Unawusandutsadi chipululu. Ukanali wokhawokha chomwecho ukundilirira Ine. Dziko lonse lasanduka chipululu chifukwa palibe wolisamalira.
12Anthu onse owononga abalalikira ku zitunda zonse za mʼchipululu. Yehova watuma ankhondo ake kudzawatha kuyambira kumalire ena a dziko mpaka ku malire enanso a dziko, ndipo palibe amene adzakhale pa mtendere.
13Anthu anafesa tirigu koma anatuta minga; anadzitopetsa kugwira ntchito koma osapeza phindu lililonse. Choncho mudzachita manyazi ndi zokolola zanu chifukwa cha mkwiyo wa Yehova.”
14“Anthu oyipa oyandikana ndi anthu anga Aisraeli, akuwalanda Aisraeliwo dziko, cholowa chimene ndinawapatsa. Nʼchifukwa chake ndidzawachotsa mʼdziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pawo.
15Komabe nditawachotsa, ndidzawachitiranso chifundo, ndipo ndidzabwezera aliyense cholowa chake ndi dziko lake.
16Ndipo ngati iwo adzaphunzira bwino njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa, namanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ monga iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, Ine ndidzawakhazikitsa pakati pa anthu anga.
17Koma ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera, Ine ndidzawuchotsa ndi kuwuwonongeratu,” akutero Yehova.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.