Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

OWERUZA 17

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Munthu wina dzina lake Mika wochokera ku dziko la mapiri la Efereimu anawuza amayi ake kuti
2“Ndinamva inu mukutemberera munthu amene anaba ndalama zanu zasiliva 1,100. Ndalamazo zili ndi ine, ndinatenga ndine.” Pamenepo amayi akewo anati, “Yehova akudalitse mwana wanga!”
3Choncho Mika anabweza ndalama 1,100 za siliva kwa amayi ake, ndipo amayi akewo anati, “Ine ndapatulira Yehova ndalama za silivazi kuti mwana wanga aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Ndiye tsopano ndikubwezera ndalamazo.”
4Tsono Mika atabweza ndalama zija kwa amayi ake, iwo anatengapo ndalama za siliva 200 namupatsa mmisiri wosula siliva. Iye anakonza fano, nasungunula siliva uja ndi kulikutira fano lija. Ndipo Mika anayika fanolo mʼnyumba mwake.
5Mikayu anali ndi kachisi, ndipo anapanga efodi ndi mafano otchedwa terafimu. Anapatula mwana wake mmodzi kuti akhale wansembe.
6Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israeli. Aliyense amachita zomwe zinamukomera.
7Ku Betelehemu mʼdziko la Yuda kunali mnyamata wina amene anali wa fuko la Levi.
8Iyeyu anachoka mu mzinda wa Betelehemu uja ku Yuda kukafuna malo ena okhala. Akuyenda, anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ku nyumba ya Mika.
9Tsono Mika anamufunsa kuti, “Mukuchokera kuti?” Ndipo iye anayakha kuti, “Ndine Mlevi wochokera ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Ndikufunafuna malo okhala.”
10Tsono Mika anati kwa iye, “Khalani ndi ine. Mukhale ngati mlangizi wanga ndi wansembe, ndipo ine ndizikupatsani ndalama za siliva khumi pa chaka komanso zovala ndi zakudya.”
11Choncho Mleviyo anavomera kuti azikhala naye, ndipo mnyamatayo anakhala ngati mmodzi mwa ana ake aamuna.
12Pambuyo pake Mika anapatula Mleviyo ndipo mnyamatayu anakhala wansembe. Tsono ankakhala mʼnyumba ya Mika.
13Ndipo Mika anati, “Tsopano ndadziwa kuti Yehova adzandikomera mtima chifukwa Mleviyu ndiye wakhala wansembe wanga.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.