Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YESAYA 61

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka. Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima, ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.
2Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake; za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake. Wandituma kuti ndikatonthoze olira.
3Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni, nkhata ya maluwa yokongola mʼmalo mwa phulusa, ndiwapatse mafuta achikondwerero mʼmalo mwa kulira. Ndiwapatse chovala cha matamando mʼmalo mwa mtima wopsinjika. Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo, yoyidzala Yehova kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.
4Adzamanganso mabwinja akale a mzinda ndipo malo amene anawonongeka kalekale aja adzakonzanso. Adzakonzanso mizinda imene inapasuka, imene yakhala yowonongeka kwa nthawi yayitali kwambiri.
5Anthu achilendo adzakutumikirani; adzazidyetsa ziweto zanu; iwo adzagwira ntchito mʼminda yanu ya mpesa.
6Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova, adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu. Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu, ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira.
7Chifukwa manyazi awo anali owirikiza; ndi kuti munalandira chitonzo ndi kutukwana, adzakondwera ndi cholowa chawo, tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza, ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo.
8“Pakuti Ine Yehova, ndimakonda chilungamo; ndimadana ndi zakuba ndi zoyipa. Anthu anga ndidzawapatsa mphotho mokhulupirika ndikupangana nawo pangano losatha.
9Ana awo adzakhala odziwika pakati pa mitundu ya anthu ndipo adzukulu awo adzakhala otchuka pakati pa anthu a mitundu ina. Aliyense wowaona adzazindikira kuti ndi anthu amene Yehova wawadalitsa.”
10Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova; moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso, ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo. Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake, ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.
11Monga momwe nthaka imameretsa mbewu ndiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala, momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamando pamaso pa mitundu yonse ya anthu.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.