Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YESAYA 50

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Yehova akuti, “Kalata imene ndinasudzulira amayi anu ili kuti? Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole, ndinakugulitsani kwa ati? Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu; amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.
2Nʼchifukwa chiyani pamene ndinabwera kudzakupulumutsani panalibe munthu? Pamene ndinayitana, nʼchifukwa chiyani panalibe wondiyankha? Kodi dzanja langa ndi lalifupi kuti nʼkulephera kukuwombolani? Kodi ndilibe mphamvu zokupulumutsirani? Ndi kudzudzula kokha ndinawumitsa nyanja yayikulu, mitsinje ndinayisandutsa chipululu; nsomba za mʼmenemo zinawola chifukwa chosowa madzi; ndipo zinafa ndi ludzu.
3Ndinaphimba thambo ndi mdima ndipo chiguduli chinakhala chofunda chake.”
4Ambuye Yehova anandiphunzitsa mawu oyenera kuyankhula kudziwa mawu olimbitsa mtima anthu ofowoka. Mmawa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa khutu langa kuti ndimve monga amachitira munthu amene akuphunzira.
5Ambuye Yehova wanditsekula makutu anga, ndipo sindinakhale munthu wowukira ndipo sindinabwerere mʼmbuyo.
6Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu; sindinawabisire nkhope yanga anthu ondinyoza ndi ondilavulira.
7Popeza Ambuye Yehova amandithandiza, sindidzachita manyazi. Tsono ndalimba mtima ngati msangalabwi, chifukwa ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.
8Wondikhalira kumbuyo ali pafupi, ndaninso amene adzandiyimba mlandu? Abwere kuti tionane maso ndi maso! Mdani wanga ndi ndani? Abweretu kuti tilimbane!
9Ambuye Yehova ndiye amene amandithandiza. Ndaninso amene adzanditsutsa? Onse adzatha ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.
10Ndani mwa inu amaopa Yehova ndi kumvera mawu a mtumiki wake? Aliyense woyenda mu mdima, popanda chomuwunikira, iye akhulupirire dzina la Yehova ndi kudalira Mulungu wake.
11Koma tsopano inu nonse amene mumasonkha moto ndi kuyatsa sakali za moto kufuna kuwononga anzanu, lowani mʼmoto wanu womwewo. Pitani mu sakali za moto zimene mwayatsa. Ndipo ine Yehova ndiye amene ndidzakugwetsereni mazunzowo.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.