Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YESAYA 47

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1“Tsika, ndi kukhala pa fumbi, iwe namwali, Babuloni; khala pansi wopanda mpando waufumu, iwe namwali, Kaldeya pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera kumugwira mosamala.
2Tenga mphero ndipo upere ufa; chotsa nsalu yako yophimba nkhope kwinya chovala chako mpaka ntchafu ndipo woloka mitsinje.
3Maliseche ako adzakhala poyera ndipo udzachita manyazi. Ndidzabwezera chilango ndipo palibe amene adzandiletse.”
4Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
5“Khala chete, ndipo lowa mu mdima, iwe namwali, Kaldeya; chifukwa sadzakutchulanso mfumukazi ya maufumu.
6Ndinawakwiyira anthu anga, osawasamalanso. Ndinawapereka manja mwako, ndipo iwe sunawachitire chifundo. Iwe unachitira nkhanza ngakhale nkhalamba.
7Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse ngati mfumukazi.’ Koma sunaganizire zinthu izi kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.
8“Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe, amene ukukhala mosatekesekawe, umaganiza mu mtima mwako kuti, ‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina. Sindidzakhala konse mkazi wamasiye, ndipo ana anga sadzamwalira.’
9Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi, zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira: ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye. Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu ngakhale ali ndi amatsenga ambiri ndi mawula amphamvu.
10Iwe unkadalira kuyipa kwako ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’ Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza, choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti, ‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’
11Ngozi yayikulu idzakugwera ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako. Mavuto adzakugwera ndipo sudzatha kuwachotsa; chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa chidzakugwera mwadzidzidzi.
12“Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako, pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo, wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako. Mwina udzatha kupambana kapena kuopsezera nazo adani ako.
13Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi! Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni. Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi zimene ziti zidzakuchitikire.
14Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi; adzapsa ndi moto. Sangathe kudzipulumutsa okha ku mphamvu ya malawi a moto. Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha; kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.
15Umu ndi mmene adzachitire amatsenga, anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako. Onse adzamwazika ndi mantha, sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.