Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YESAYA 4

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Tsiku limenelo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi, nʼkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu, ndi kuvala zovala zathu; inu mungotilola kuti tidziyitanidwa ndi dzina lanu. Tichotseni manyazi aumbeta!”
2Tsiku limenelo Nthambi ya Yehova idzakhala yokongola ndi yaulemerero, ndipo chipatso cha mʼdziko chidzakhala chonyaditsa ndi chopereka ulemerero kwa onse opulumuka mu Israeli.
3Iwo amene adzatsale mu Ziyoni, amene adzatsalire mu Yerusalemu, adzatchedwa oyera, onse amene mayina awo alembedwa pakati pa anthu amoyo okhala mu Yerusalemu.
4Ambuye adzasambitsa akazi a Ziyoni ndi kuchotsa zonyansa zawo. Adzatsuka magazi amene anakhetsedwa mu Yerusalemu ndi mzimu wachiweruzo ndiponso mzimu wamoto.
5Tsono Yehova adzayika mtambo wake pamwamba ponse pa phiri la Ziyoni, ndipo pa onse amene asonkhana masana padzakhala mtambo wa utsi ndipo usiku padzakhala malawi amoto. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Yehova.
6Ulemerero wake udzakhala mthunzi wothawiramo kutentha kwa masana, udzakhala malo opeweramo mphepo ndi owusiramo mvula.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.