Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YESAYA 39

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani mfumu ya ku Babuloni anatumiza nthumwi kwa Hezekiya nawapatsira makalata ndi mphatso, pakuti anamva za kudwala kwake ndi kuti anachira.
2Hezekiya anawalandira mwasangala ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo siliva, golide, zokometsera zakudya, mafuta abwino kwambiri, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene zinkapezeka mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse ka mʼnyumba yaufumu kapena mu ufumu wake onse kamene sanawaonetse.
3Tsono mneneri Yesaya anapita kwa mfumu Hezekiya ndipo anamufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani chiyani, ndipo anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”
4Mneneri anafunsanso kuti, “Kodi mʼnyumba yanu yaufumu anaonamo chiyani?” Hezekiya anati, “Anaona chilichonse cha mʼnyumba yanga yaufumu. Palibe ndi chimodzi chomwe za mʼnyumba yosungiramo chuma changa chimene sindinawaonetse.”
5Pamenepo Yesaya anati kwa Hezekiya, “Imvani mawu a Yehova Wamphamvuzonse:
6Yehova akuti, nthawi idzafika ndithu pamene zonse za mʼnyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu anazisonkhanitsa mpaka lero lino, zidzatengedwa kupita nazo ku Babuloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe.
7Ndipo ena mwa ana anu, obala inu amene adzatengedwanso, ndipo adzawasandutsa adindo ofulidwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Babuloni.”
8Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhula ndi abwino.” Ponena izi iye ankaganiza kuti, “Padzakhala mtendere ndi chitetezo masiku a moyo wanga onse.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.