Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YESAYA 35

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala; dziko lowuma lidzakondwa ndi kuchita maluwa.
2Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wa Mulungu wathu.
3Limbitsani manja ofowoka, limbitsani mawondo agwedegwede;
4nenani kwa a mitima yamantha kuti; “Limbani mtima, musachite mantha; Mulungu wanu akubwera, akubwera kudzalipsira; ndi kudzabwezera chilango adani anu; akubwera kudzakupulumutsani.”
5Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.
6Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala, ndipo osayankhula adzayimba mokondwera. Akasupe adzatumphuka mʼchipululu ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma,
7mchenga wotentha udzasanduka dziwe, nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe. Pamene panali mbuto ya ankhandwe padzamera udzu ndi bango.
8Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu; ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika. Anthu odetsedwa sadzayendamo mʼmenemo; zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.
9Kumeneko sikudzakhala mkango, ngakhale nyama yolusa sidzafikako; sidzapezeka konse kumeneko. Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu.
10Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera. Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba; kumeneko adzakondwa mpaka muyaya. Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe, ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.