Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YESAYA 32

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Taonani, kudzakhala mfumu ina imene idzalamulira mwachilungamo, ndipo akalonga ake adzaweruza molungama.
2Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe, adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu, ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.
3Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka, ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.
4Anthu a mtima wopupuluma adzadziwa ndi kuchita zinthu mofatsa, ndipo anthu ovutika kuyankhula adzayankhula mosadodoma ndi momveka.
5Chitsiru sichidzatchedwanso munthu waulemu wake ndipo munthu woyipa sadzalemekezedwa.
6Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru, amaganiza kuchita zoyipa: Iye amachita zoyipira Mulungu, ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova; anjala sawapatsa chakudya ndipo aludzu sawapatsa madzi.
7Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso, iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa. Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.
8Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino, Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.
9Khalani maso, inu akazi amene mukungokhala wopanda kulingalira kuti kunja kulinji ndipo imvani mawu anga. Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikunena!
10Pakapita chaka ndi masiku pangʼono inu akazi amatama mudzanjenjemera; chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika ndipo zipatso sizidzaoneka.
11Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu; ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu. Vulani zovala zanu, ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu.
12Dzigugudeni pachifuwa mwachisoni chifukwa minda yachonde, ndi mphesa yawonongeka.
13Mʼdziko la anthu anga mwamera minga ndi mkandankhuku. Zoona, mulilire nyumba zonse zachikondwerero ndi mzinda uno umene unali wachisangalalo.
14Nyumba yaufumu idzasiyidwa, mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu; malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya. Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.
15Yehova adzatipatsa mzimu wake, ndipo dziko lachipululu lidzasanduka munda wachonde, ndipo munda wachonde udzakhala ngati nkhalango.
16Tsono mʼchipululu mudzakhala chiweruzo cholungama ndipo mʼminda yachonde mudzakhala chilungamo.
17Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo; zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.
18Anthu anga adzakhala mʼmidzi yamtendere, mʼnyumba zodalirika, ndi malo osatekeseka a mpumulo.
19Ngakhale nkhalango idzawonongedwa ndi matalala ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi,
20inutu mudzakhala odalitsika ndithu. Mudzadzala mbewu zanu mʼmbali mwa mtsinje uliwonse, ndipo ngʼombe zanu ndi abulu anu zidzadya paliponse.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.