Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YESAYA 27

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Tsiku limenelo, Yehova ndi lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu, adzalanga Leviyatani chinjoka chothawa chija, Leviyatani chinjoka chodzikulunga; adzapha chirombo choopsa cha mʼnyanja.
2Tsiku limenelo Yehova adzati, “Tidzayimba nyimbo ya munda wamphesa wobereka bwino:
3Ine, Yehova, ndimawuyangʼanira; ndimawuthirira nthawi zonse. Ndimawulondera usana ndi usiku kuti wina angawononge.
4Ine sindinakwiye. Ngati mkandankhuku ndi minga zikanaoneka ndikanalimbana nazo! Ndikachita nazo nkhondo; ndikanazitentha zonse ndi moto.
5Koma ngati apo ayi, abweretu kwa Ine adani angawo kuti ndidzawateteze; apangane nane za mtendere, ndithu, apangane nane za mtendere.”
6Masiku akubwerawo Yakobo adzazika mizu, Israeli adzaphukira ndi kuchita maluwa, ndipo adzadzaza dziko lonse lapansi ndi zipatso.
7Kodi Yehova anakantha Israeli ngati momwe anakanthira anthu amene anazunza Israeli? Kapena kodi Yehova anapha Israeli ngati mmene anthu ena anaphera Israeli?
8Yehova mwawalanga powapirikitsa ndi kuwatumiza ku ukapolo, mwawachotsa ndi mpweya wanu woopsa, monga zimachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kummawa.
9Yehova adzakhululuka kulakwa kwa Yakobo. Iwo adzaonetsa kuti alapadi pamene adzaphwanya miyala yonse ya guwa lachikunja, ngati mmene anthu amaphwanyira miyala yanjereza mpaka kukhala ngati fumbi lokhalokha. Sipadzapezekanso mafano a Asera kapena maguwa ofukiza lubani.
10Mzinda wamalinga uja wasanduka bwinja, wasanduka malo osiyidwa, ndi kutayidwa ngati chipululu; kumeneko amadyetselako ana angʼombe kumeneko zimapumulako ziweto ndi kumwetula nthambi za mitengo kotheratu.
11Pamene nthambi za mitengoyo zauma, zimathyoka ndipo amayi amabwera nazitola ndi kuzisandutsa nkhuni. Pakuti awa ndi anthu opanda nzeru; kotero Mulungu amene anawapanga sadzachitira chisoni, ndipo Mlengi wawo sawakomera mtima.
12Tsiku limenelo Yehova adzasonkhanitsa pamodzi anthu ake mmodzimmodzi kumalo opunthira tirigu, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Igupto.
13Ndipo tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira. Amene akuzunzika ku Asiriya iwo amene ali ku ukapolo ku Igupto adzabwera ndi kudzalambira Yehova pa phiri lopatulika mu Yerusalemu.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.