Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

YESAYA 18

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Tsoka kwa anthu a ku Kusi. Kumeneko kumamveka mkokomo wa mapiko a dzombe.
2Dziko limenelo limatumiza akazembe pa mtsinje wa Nailo, mʼmabwato amabango amene amayandama pa madzi, ndikunena kuti, “Pitani, inu amithenga aliwiro, kwa mtundu wa anthu ataliatali a khungu losalala, ndi woopedwa ndi anthu. Akazembe anatumidwa ku dziko la anthu amphamvu ndi logonjetsa anthu ena. Dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.”
3Inu nonse anthu a pa dziko lonse, inu amene mumakhala pa dziko lapansi, pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri yangʼanani, ndipo pamene lipenga lilira mumvere.
4Pakuti Yehova akunena kwa ine kuti, “Ndili chikhalire ku malo anga kuno, ndidzakhala chete, ndi kumangoyangʼana, monga momwe dzuwa limawalira nthawi yotentha, monganso momwe mame amagwera usiku pa nthawi yotentha yokolola.”
5Pakuti, anthu asanayambe kukolola, maluwa atayoyoka ndiponso mphesa zitayamba kupsa, Iye adzadula mphukira ndi mipeni yosadzira, ndipo adzadula ndi kuchotsa nthambi zotambalala.
6Mitembo ya anthu ankhondo adzasiyira mbalame zamʼmapiri zodya nyama ndiponso zirombo zakuthengo; mbalame zidzadya mitemboyo nthawi yonse ya chilimwe, ndipo zirombo zidzayidya pa nthawi yonse yachisanu.
7Pa nthawi imeneyo anthu adzabwera ndi mphatso kwa Yehova Wamphamvuzonse, zochokera kwa anthu ataliatali ndi osalala, kuchokera kwa mtundu wa anthu woopedwa ndi anthu apafupi ndi akutali omwe, mtundu wa anthu amphamvu ndi a chiyankhulo chachilendo, anthu amene dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje. Adzabwera nazo mphatso ku Phiri la Ziyoni, ku malo a Dzina la Yehova Wamphamvuzonse.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.