Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

HOSEYA 6

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1“Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova. Iye watikhadzula, koma adzatichiritsa. Iye wativulaza, koma adzamanga mabala athu.
2Pakapita masiku awiri adzatitsitsimutsa; pa tsiku lachitatu Iye adzatiukitsa kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.
3Tiyeni timudziwe Yehova, tiyeni tilimbike kumudziwa Iye. Adzabwera kwa ife mosakayikira konse ngati kutuluka kwa dzuwa; adzabwera kwa ife ngati mvula ya mʼchilimwe, ngati mvula ya nthawi yamphukira imene imakhathamiritsa nthaka.”
4Iwe Efereimu, kodi ndichite nawe chiyani? Kodi ndichite nawe chiyani, iwe Yuda? Chikondi chanu chili ngati nkhungu yammawa, ngati mame a mmamawa amene amakamuka msanga.
5Choncho ndakuwazani ngati nkhuni kudzera mwa aneneri anga, ndakuphani ndi mawu a pakamwa panga; chigamulo changa chinangʼanima ngati mphenzi pa inu.
6Pakuti Ine ndimafuna chifundo osati nsembe, ndi kudziwa Mulungu kulekana ndi nsembe zopsereza.
7Monga Adamu, anthuwa aphwanya pangano langa, iwo sanakhulupirike kwa Ine.
8Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoyipa, okhala ndi zizindikiro za kuphana.
9Monga momwe mbala zimadikirira anthu, magulu a ansembe amachitanso motero; iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu, kupalamula milandu yochititsa manyazi.
10Ndaona chinthu choopsa kwambiri mʼnyumba ya Israeli. Kumeneko Efereimu akuchita zachiwerewere, ndipo Israeli wadzidetsa.
11“Kunenanso za iwe Yuda, udzakolola chilango. “Pamene ndiwabwezere anthu anga zinthu zabwino.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.