Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

HOSEYA 13

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Kale Efereimu ankati akayankhula, anthu ankanjenjemera; anali wolemekezeka mu Israeli. Koma analakwa popembedza Baala, motero anafa.
2Tsopano akunka nachimwirachimwirabe; akudzipangira mafano pogwiritsa ntchito siliva wawo, zifanizo zopangidwa mwaluso, zonsezo zopangidwa ndi amisiri. Amanena za anthu awa kuti, “Amatenga munthu ndi kumupereka nsembe ndipo amapsompsona fano la mwana wangʼombe.”
3Choncho adzakhala ngati nkhungu yammawa, ngati mame amene amakamuka msanga, ngati mungu wowuluka kuchokera pa malo opunthira tirigu, ngati utsi umene ukutulukira pa zenera.
4Koma Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mu Igupto. Simuyenera kudziwa Mulungu wina, koma Ine ndekha, palibe Mpulumutsi wina kupatula Ine.
5Ndinakusamalira mʼchipululu, mʼdziko lotentha kwambiri.
6Pamene ndinawadyetsa, iwo anakhuta; iwo atakhuta anayamba kunyada; ndipo anandiyiwala Ine.
7Motero ndidzawalumphira ngati mkango, ndidzawabisalira mu msewu ngati kambuku.
8Ngati chimbalangondo cholandidwa ana ake, ndidzawambwandira ndi kuwathyolathyola. Ndidzawapwepweta ngati mkango; chirombo chakuthengo chidzawakhadzula.
9“Iwe Israeli, wawonongedwa, chifukwa ukutsutsana ndi Ine, ukutsutsana ndi mthandizi wako.
10Kodi mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse? Olamulira ako a mʼmizinda yonse ali kuti, amene iwe unanena za iwo kuti, ‘Patseni mfumu ndi akalonga?’
11Choncho Ine ndinakupatsani mfumu mwachipseramtima, ndipo ndinayichotsa mwaukali.
12Kulakwa kwa Efereimu kwasungidwa, machimo ake alembedwa mʼbuku.
13Zowawa zonga za mayi pa nthawi yobala mwana zamugwera, koma iye ndi mwana wopanda nzeru, pamene nthawi yake yobadwa yafika iyeyo safuna kutuluka mʼmimba mwa amayi ake.
14“Ndidzawapulumutsa ku mphamvu ya manda; ndidzawawombola ku imfa. Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? “Sindidzachitanso chifundo,
15ngakhale Efereimu akondwe pakati pa abale ake, mphepo ya kummawa yochokera kwa Yehova idzabwera, ikuwomba kuchokera ku chipululu. Kasupe wake adzaphwa ndipo chitsime chake chidzawuma. Chuma chake chonse chamtengowapatali chidzafunkhidwa ndipo chidzatengedwa.
16Anthu a ku Samariya adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo, chifukwa anawukira Mulungu wawo. Adzaphedwa ndi lupanga; ana awo adzaphedwa mowamenyetsa pansi, akazi awo oyembekezera adzatumbulidwa pa mimba.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.