Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

EZARA 1

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi mfumu ya Perisiya, pofuna kukwaniritsa zimene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anayika maganizo mu mtima mwa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mʼdziko lake lonse ndi mawu apakamwa ngakhalenso ochita kulemba.
2Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti, “ ‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda.
3Aliyense wa inu amene ali wa Yehova, Mulungu wakeyo akhale naye. Tsono aliyense wa inu apite ku Yerusalemu, mʼdziko la Yuda kuti akamange Nyumba ya Yehova, Mulungu wa Israeli. Iyeyu ndi Mulungu amene ali mu Yerusalemu.
4Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’ ”
5Choncho atsogoleri a mabanja afuko la Yuda ndi la Benjamini komanso ansembe ndi Alevi, aliyense amene Mulungu anawutsa mtima wake, anayamba kukonzeka kupita kukamanga Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.
6Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija.
7Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake.
8Koresi, mfumu ya ku Perisiya inatulutsa ziwiyazi ndi kuzipereka kwa Miteridati, msungichuma amene anaziwerenga pamaso pa Sesibazara nduna yayikulu ya dziko la Yuda.
9Chiwerengerochi chinali motere: Mabeseni agolide 30 mabeseni asiliva 1,000 a zopereka 29
10timiphika tagolide 230 timiphika tasiliva 410 ziwiya zina 1,000.
11Ziwiya zonse zagolide ndi siliva pamodzi zinalipo 5,400. Zonsezi ndi zimene Sezi-Bazara anabwera nazo pamene otengedwa ukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babuloni.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.