Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

EKSODO 31

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Ndipo Yehova anati kwa Mose,
2“Taona, ndasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda.
3Ndipo ndamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi:
4Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa,
5kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja.
6Ndasankhanso Oholiabu mwana wa Ahisamaki wa fuko la Dani. Ndiponso ndapereka nzeru kwa anthu aluso motero adzagwira ntchito zonse zimene ndakulamulira kuti zichitike monga izi:
7Kupanga tenti ya msonkhano, bokosi laumboni pamodzi ndi chophimbira chake, ndiponso zonse za mu tenti,
8tebulo ndi zida zake, choyikapo nyale cha golide wabwino kwambiri ndi ziwiya zake zonse, guwa lofukizirapo lubani,
9guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, beseni ndi nsichi yake,
10ndiponso zovala zonse zolukidwa, zovala zopatulika za Aaroni wansembe pamodzi ndi za ana ake, zovala pamene akutumikira monga ansembe,
11ndiponso mafuta odzozera ndi lubani wonunkhira wa ku malo opatulika. Iwo azipanga monga momwe Ine ndinakulamulira.”
12Ndipo Yehova anati kwa Mose,
13“Uza ana a Israeli kuti azisunga Masabata anga. Ichi chidzakhala chizindikiro pakati pa inu ndi Ine pamodzi ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo, chosonyeza kuti Ine ndine amene ndimakuyeretsani.
14“Motero muzisunga tsiku la Sabata chifukwa ndi loyera kwa inu. Aliyense amene adetsa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.
15Mugwire ntchito kwa masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, lopuma, tsiku lopatulika la Yehova. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa.
16Aisraeli onse komanso zidzukulu zawo mʼtsogolo azidzasunga tsiku la Sabata ngati pangano lamuyaya.
17Tsiku la Sabata lidzakhala chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi Aisraeli chosonyeza kuti Yehova analenga za kumwamba ndi dziko lapansi kwa masiku asanu ndi limodzi ndi kuti pa tsiku lachisanu ndi chiwiri analeka kugwira ntchito napumula.”
18Yehova atamaliza kuyankhula ndi Mose pa phiri la Sinai, anamupatsa Mose miyala iwiri yaumboni, imene Mulungu analembapo ndi chala chake.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.